Psalms 118

1Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

2Israeli anene kuti:
“Chikondi chake ndi chosatha.”
3Banja la Aaroni linene kuti,
“Chikondi chake ndi chosatha.”
4Iwo amene amaopa Yehova anene kuti:
“Chikondi chake ndi chosatha.”

5Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova,
ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
6Yehova ali nane; sindidzachita mantha.
Munthu angandichite chiyani?
7Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa.
Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.

8Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
kusiyana ndi kudalira munthu.
9Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
kusiyana ndi kudalira mafumu.

10Anthu a mitundu yonse anandizinga,
koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
11Anandizinga mbali zonse,
koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
12Anandizinga ngati njuchi,
koma anatha msanga ngati moto wapaminga;
mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

13Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa,
koma Yehova anandithandiza.
14Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.

15Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”

17Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18Yehova wandilanga koopsa,
koma sanandipereke ku imfa.

19Tsekulireni zipata zachilungamo,
kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20Ichi ndicho chipata cha Yehova
chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
mwakhala chipulumutso changa.

22Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wasanduka wapangodya;
23Yehova ndiye wachita zimenezi
ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

25Inu Yehova, tipulumutseni;
Yehova, tipambanitseni.
26Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.
Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
27Yehova ndi Mulungu,
ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife.
Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu,
mpaka ku nyanga za guwa.

28Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.

29Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
Copyright information for NyaCCL